Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 18:35 - Buku Lopatulika

35 Pilato anayankha, Ndili ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe aakulu anakupereka kwa ine; wachita chiyani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Pilato anayankha, Ndili ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe aakulu anakupereka kwa ine; wachita chiyani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Pilato adati, “Ine ndine Myuda kodi? Anthu a mtundu wako womwe ndiponso akulu a ansembe ndiwo akupereka kwa ine. Udachita chiyani?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Pilato anayankha kuti, “Kodi iwe ukuganiza kuti ine ndine Myuda? Ndi anthu ako ndi akulu a ansembe ako amene akupereka iwe kwa ine. Kodi walakwanji?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 18:35
14 Mawu Ofanana  

Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ochokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mzinda uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ake, nalumikiza maziko ake.


Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


Yesu anayankha, Kodi munena ichi mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine?


Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.


Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.


Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu?


Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a chilamulo chao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga.


Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa