Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 18:25 - Buku Lopatulika

25 Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa ophunzira ake kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa ophunzira ake kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Simoni Petro anali chililibe akuwotha nao moto. Tsono ena adamufunsa kuti, “Kodi iwenso sindiwe mmodzi mwa ophunzira a munthu uja?” Petro adakana, adati, “Iyai.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Pamene Simoni Petro anali chiyimirire kuwotha moto, anafunsidwa kuti, “Kodi iwe si mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 18:25
13 Mawu Ofanana  

Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka.


Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.


Ndipo pamene Petro anali pansi m'bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;


Ndipo pamene adasonkha moto m'kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro anakhala pakati pao.


Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwake kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye.


Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa