Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 18:17 - Buku Lopatulika

17 Pamenepo mdzakazi wapakhomoyo ananena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa ophunzira a munthu uyu? Iyeyu ananena, Sindine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Pamenepo mdzakazi wapakhomoyo ananena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa ophunzira a munthu uyu? Iyeyu ananena, Sindine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Mtsikanayo adafunsa Petro kuti, “Kodi inu sindinunso mmodzi mwa ophunzira a munthuyu?” Iye adati, “Ineyo? Iyai.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Mtsikanayo anafunsa Petro kuti, “Kodi iwe sindiwe mmodzi wa ophunzira a Munthu uyu?” Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 18:17
11 Mawu Ofanana  

Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.


Ndipo pamenepo anamgwira Iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutali.


koma Petro anaima kukhomo kunja. Chifukwa chake wophunzira winayo amene anadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka nalankhula ndi wapakhomo, nalowetsa Petro.


Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa ophunzira ake kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine.


Anayankha Iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudasi yemwe, wompereka Iye, anaima nao pamodzi.


Yesu anayankha, Nati, Ndine; chifukwa chake ngati mufuna Ine, lekani awa amuke;


Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa anaankhosa anga.


Ndipo m'mene anagogoda pa chitseko cha pakhomo, anadza kudzavomera mdzakazi, dzina lake Roda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa