Yohane 16:17 - Buku Lopatulika17 Mwa ophunzira ake tsono anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundione; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, chifukwa ndimuka kwa Atate? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Mwa ophunzira ake tsono anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, chifukwa ndimuka kwa Atate? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Ophunzira ake ena adayamba kufunsana kuti, “Kodi nchiyani akutiwuzachi? Akuti, ‘Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona.’ Akutinso, ‘Chifukwa ndikupita kwa Atate.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ” Onani mutuwo |