Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 12:42 - Buku Lopatulika

42 Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze, kuti angaletsedwe m'sunagoge,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereza, kuti angaletsedwe m'sunagoge,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Komabe ambiri mwa atsogoleri ao omwe adakhulupirira Yesu. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sankanena zimenezo poyera. Ankaopa kuti angaŵadule ku mpingo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Komabe pa nthawi yomweyi ambiri ngakhale atsogoleri anakhulupirira Iye. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sanavomereze chikhulupiriro chawo chifukwa amaopa kuti angawatulutse mʼsunagoge;

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:42
25 Mawu Ofanana  

Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.


Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhale chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiope Ine konse?


Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.


Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Ababiloni, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke.


Chifukwa chake yense amene adzavomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.


Ndipo ndinena kwa inu, Amene aliyense akavomereza Ine pamaso pa anthu, inde, Mwana wa Munthu adzamvomereza iye pamaso pa angelo a Mulungu;


Ndipo Pilato anaitana ansembe aakulu, ndi akulu, ndi anthu, asonkhane,


Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu.


Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye.


pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimatea, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Chifukwa chake anadza, nachotsa mtembo wake.


Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


Chinkana anatero panalibe munthu analankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuopa Ayuda.


Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?


Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.


Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.


Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu a milandu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.


pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m'kamwa avomereza kutengapo chipulumutso.


Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.


M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa