Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 12:38 - Buku Lopatulika

38 kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati, Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu? Ndipo mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa yani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati, Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu? Ndipo mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa yani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaaneneratu kuti, “Ambuye, ndani wakhulupirira kulalika kwathu? Ndani wazindikira mphamvu za Ambuye pa zimenezi?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Izi zinakwaniritsa mawu a mneneri Yesaya kuti: “Ambuye, wakhulupirira uthenga wathu ndani, ndipo ndi kwa yani komwe mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:38
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesaya mneneri mwana wa Amozi, anapemphera pa ichi, nafuulira Kumwamba.


Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,


Chilungamo changa chili pafupi, chipulumutso changa chamuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.


Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?


Ndani wamvera uthenga wathu? Ndi mkono wa Yehova wavumbulukira yani?


Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti,


Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.


Ndipo pamene anampachika Iye, anagawana zovala zake ndi kulota maere:


Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirire Iye;


Chifukwa cha ichi sanathe kukhulupirira, pakuti Yesaya anatinso,


Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi.


Koma sanamvere Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife?


Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati, Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifune; ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunse.


koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.


kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsane ndi thupi ndi mwazi:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa