Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 12:29 - Buku Lopatulika

29 Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Panali khamu la anthu pamenepo. Tsono pamene adamva mauwo, adati, “Kwagunda bingu.” Koma ena adati, “Mngelo walankhula naye.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Gulu la anthu lomwe linali pamenepo litamva linati, “Kwagunda bingu,” ena anati, “Mngelo wayankhula kwa Iye.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:29
12 Mawu Ofanana  

Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu? Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?


Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.


Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.


Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima duu, atamvadi mau, koma osaona munthu.


Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.


Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao;


Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinai, chikunena, ngati mau a bingu, Idza.


Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala paguwa la nsembe, nauponya padziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa