Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 11:37 - Buku Lopatulika

37 Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sakanatha kodi kuchita kuti asafe ameneyunso?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sanakhoza kodi kuchita kuti sakadafa ameneyunso?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Koma ena mwa iwo adati, “Munthu uyu suja adapenyetsa munthu wosapenya uja? Monga sakadatha kuchitapo kanthu kuti Lazaroyu asafe?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Koma ena a iwo anati, “Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:37
9 Mawu Ofanana  

Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse.


Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.


Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.


Ndipo mmodzi wa ochita zoipa anapachikidwawo anamchitira Iye mwano nanena, Kodi suli Khristu Iwe? Udzipulumutse wekha ndi ife.


Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.


Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa