Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 11:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 komabe chifukwa cha inu ndikukondwera kuti Ine kunalibe kumeneko, kuti choncho mukakhulupirire. Tiyeni tipiteko.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe kumeneko; koma kuti mukakhulupirire tiyeni tipiteko.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:15
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, chifukwa kuti Ine ndili ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa mbeu zako, chifukwa cha Abrahamu kapolo wanga.


Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, ndi pa zake zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwejipito chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zake zonse, m'nyumba ndi m'munda.


Sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa.


Taona, iwo angasonkhanitse pamodzi, koma si ndi Ine; aliyense amene adzasonkhana pamodzi akangane ndi iwe adzagwa chifukwa cha iwe.


Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, ndidzachita chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.


Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.


Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.


Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.


Yesu anayankha nati, Mau awa sanafike chifukwa cha Ine, koma cha inu.


Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.


Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.


Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.


Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.


Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa