Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 9:5 - Buku Lopatulika

5 Ndiye amene asuntha mapiri, osachidziwa iwo, amene amagubuduza mu mkwiyo wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndiye amene asuntha mapiri, osachidziwa iwo, amene amagubuduza mu mkwiyo wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Iyeyo amasendeza mapiri, iwo osadziŵako, amaŵagubuduza ali wokwiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa, ndipo amawagubuduza ali wokwiya.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 9:5
23 Mawu Ofanana  

Kumanda kuli padagu pamaso pake, ndi kuchionongeko kusowa chophimbako.


Munthu atambasulira dzanja lake kumwala; agubuduza mapiri kuyambira kumizu.


Pakuti asamalira ntchito zao, nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.


Tsanulira mkwiyo wako wosefuka, nupenyerere aliyense wodzikuza ndi kumchepetsa.


Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze? Zilizonse pansi pa thambo ponse ndi zanga.


Munatumphatumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu? Ngati anaankhosa, zitunda inu?


Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.


Dziko lapansi linagwedezeka, inde thambo linakha pamaso pa Mulungu; Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israele.


Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?


Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.


Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.


Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.


Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.


Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.


Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;


ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.


Ndipo kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kuchoka m'malo mwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa