Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 9:3 - Buku Lopatulika

3 Akafuna Iye kutsutsana naye, sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa chikwi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Akafuna Iye kutsutsana naye, sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa chikwi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kodi wina aliyense angathe kutsutsana ndi Mulungu? Ai sangathe kutsutsana naye, chifukwa Mulungu ali ndi mafunso ambiri osayankhika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye, Iye sangamuyankhe munthuyo ngakhale mawu amodzi omwe.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 9:3
18 Mawu Ofanana  

Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse; mundidziwitse chifukwa cha kutsutsana nane.


Ndaniyo adzatsutsana nane? Ndikakhala chete, ndidzapereka mzimu wanga.


Mutsutsana ndi Iye chifukwa ninji? Popeza pa zake zonse sawulula chifukwa.


Pakuti Mulungu alibe chifukwa cha kulingiriranso za munthu, kuti afike kwa Iye kudzaweruzidwa.


Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse? Wochita makani ndi Mulungu ayankhe.


Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayankha; inde kawiri, koma sindionjezanso.


Nanga ine tsono ndidzamyankha bwanji, ndi kusankha mau anga akutsutsana ndi Iye?


Chinkana ndikhala wolungama, pakamwa panga padzanditsutsa; chinkana ndikhala wangwiro, padzanditsutsa wamphulupulu.


Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.


Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.


Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?


Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi.


m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa