Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 9:2 - Buku Lopatulika

2 Zoona, ndidziwa kuti chili chotero. Koma munthu adzakhala wolungama bwanji kwa Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Zoona, ndidziwa kuti chili chotero. Koma munthu adzakhala wolungama bwanji kwa Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Inde, ndikudziŵa kuti zimenezi ndi zoona, koma nanga munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona. Koma munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?

Onani mutuwo Koperani




Yobu 9:2
13 Mawu Ofanana  

Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,


Yehova Mulungu wa Israele, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tili pamaso panu m'kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi.


Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?


Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala; ndi nyenyezi siziyera pamaso pake;


Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi, wa chibale cha Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.


Ndine woyera ine, wopanda kulakwa, ndine wosapalamula, ndilibe mphulupulu.


Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama, ndipo Mulungu wandichotsera choyenera ine


Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu? Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wake?


Pamenepo Yobu anayankha, nati,


Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?


Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.


chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa