Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 7:9 - Buku Lopatulika

9 Mtambo wapita watha, momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mtambo wapita watha, momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka, momwemonso munthu woloŵa ku manda sabwerako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka, momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 7:9
14 Mawu Ofanana  

Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.


Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.


ndisanachoke kunka kumene sindikabweranso, ku dziko la mdima ndi la mthunzi wa imfa.


Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji? Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji?


Pakuti zitafika zaka zowerengeka, ndidzamuka kunjira imene sindibwererako.


Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga; ndikayala pogona panga mumdima.


Chidzatsikira kumipingiridzo ya kumanda, pamene tipumulira pamodzi kufumbi.


Pakuti ndikadagona pansi pomwepo ndi kukhala chete; ndikanagona tulo; pamenepo ndikadaona popumula;


Anditembenuzira zondiopsa, auluza ulemu wanga ngati mphepo; ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo.


Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi, afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yake;


Ndiloleni, kuti nditsitsimuke, ndisanamuke ndi kukhala kuli zii.


Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; chifukwa chake Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa chikumbukiro chao chonse.


Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa