Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 7:7 - Buku Lopatulika

7 Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo, diso langa silidzaonanso chokoma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo, diso langa silidzaonanso chokoma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya. Masiku abwino sindidzaŵaonanso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya; sindidzaonanso masiku achisangalalo.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 7:7
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.


Mukumbukire mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu;


Masiku anga satsala owerengeka nanga? Lindani. Bandilekani kuti nditsitsimuke pang'ono,


Mukumbukire kuti mwandiumba ngati dothi; ndipo kodi mudzandibwezera kufumbi?


Ndinyansidwa nao moyo wanga; sindidzakhala ndi moyo chikhalire; mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe.


Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma; athawa osaona chokoma.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza, ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.


Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha; kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse.


Ndipo anakumbukira kuti iwo ndiwo anthu; mphepo yopita yosabweranso.


Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi; munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?


Kumbukirani, Ambuye, chotonzera atumiki anu; ndichisenza m'chifuwa mwanga chochokera kumitundu yonse yaikulu ya anthu.


Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire Ine, mundibwezere chilango pa ondisautsa ine; musandichotse m'chipiriro chanu; dziwani kuti chifukwa cha Inu ndanyozedwa.


inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa