Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 7:1 - Buku Lopatulika

1 Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno? Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno? Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Moyo wa munthu pa dziko lapansi ndi wa ntchito yakalavulagaga. Masiku ake ali ngati a munthu waganyu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi? Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu?

Onani mutuwo Koperani




Yobu 7:1
16 Mawu Ofanana  

Mundikonzeranso mboni zonditsutsa, ndi kundichulukitsira mkwiyo wanu; nkhondo yobwerezabwereza yandigwera.


Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.


Koma munthu abadwira mavuto, monga mbaliwali zikwera ziuluzika.


Monga kapolo woliralira mthunzi, monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,


Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa, ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati; ndidziwe malekezero anga.


Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udyo sudzapulumutsa akuzolowerana nao.


Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Mowabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang'onong'ono ndi achabe.


Pakuti Ambuye anatero kwa ine, Chisanapite chaka malinga ndi zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wonse wa Kedara udzagoma;


Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.


Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse.


Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira chaka adadzigulitsa kwa iye kufikira chaka choliza lipenga; ndipo mtengo wake ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.


Musamayesa nchosautsa, pomlola akuchokereni waufulu; popeza anakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi monga wolipidwa wakulandira chowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa