Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 6:9 - Buku Lopatulika

9 Chimkomere Mulungu kundiphwanya, alole dzanja lake lindilikhe!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Chimkomere Mulungu kundiphwanya, alole dzanja lake lindilikhe!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Achikhala kudaamkomera Mulungu kuti anditswanye, achikhala adaandimenya ndi dzanja lake, nkundiwonongeratu!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye, kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu!

Onani mutuwo Koperani




Yobu 6:9
16 Mawu Ofanana  

Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.


Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.


Koma maso a oipa adzagoma, ndi pothawirapo padzawasowa, ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao.


Ha? Mukadandibisa kumanda, mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.


Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.


Ha! Ndikadakhala nacho chimene ndichipempha, Mulungu akadandipatsa chimene ndichilira!


Chinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini, ndipeputsa moyo wanga.


Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.


Pokhala panga pachotsedwa, pandisunthikira monga hema wa mbusa; Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba; Iye adzandidula ine poomberapo; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.


Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.


Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.


Ndipo m'masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa