Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 6:8 - Buku Lopatulika

8 Ha! Ndikadakhala nacho chimene ndichipempha, Mulungu akadandipatsa chimene ndichilira!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ha! Ndikadakhala nacho chimene ndichipempha, Mulungu akadandipatsa chimene ndichilira!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 “Achikhala ndidaalandira chomwe ndikufuna, achikhala Mulungu adaandipatsa chimene ndikukhumba!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha, chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera,

Onani mutuwo Koperani




Yobu 6:8
10 Mawu Ofanana  

Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.


Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.


wakuyembekezera imfa, koma kuli zii, ndi kuikumba koposa chuma chobisika,


wakusekerera ndi chimwemwe ndi kukondwera pakupeza manda?


Zimene moyo wanga ukana kuzikhudza zikunga chakudya chosakolera kwa ine.


Chimkomere Mulungu kundiphwanya, alole dzanja lake lindilikhe!


Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba chipulumutso chanu: Ndinayembekezera mau anu.


Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa