Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 5:4 - Buku Lopatulika

4 Ana ake akhala otekeseka, napsinjika kuchipata, wopanda wina wakuwapulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ana ake akhala otekeseka, napsinjika kuchipata, wopanda wina wakuwapulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ana ake alibe nchitetezo chomwe, amaŵapondereza m'bwalo lamilandu, palibe wina aliyense woŵapulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe; amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 5:4
16 Mawu Ofanana  

ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.


chinkana mudziwa kuti sindili woipa, ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu?


Ana ake adzapempha aumphawi awakomere mtima; ndi manja ake adzabweza chuma chake.


Akachuluka ana ake, ndiko kuchulukira lupanga, ndi ana ake sadzakhuta chakudya.


Chinkana ana ako anamchimwira Iye, ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao;


Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu.


Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.


kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.


Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;


Nzeru italikira chitsiru; satsegula pakamwa kubwalo.


Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.


Munthu akathawira umodzi wa mizinda iyi, aziima polowera pa chipata cha mzindawo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mzindawo; pamenepo azimlandira kumzinda kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa