Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 4:4 - Buku Lopatulika

4 Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa, walimbitsanso maondo otewa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa, walimbitsanso maondo otewa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mau ako adathandiza munthu wofuna kugwa, adachirikiza munthu wotha mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa; unachirikiza anthu wotha mphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 4:4
15 Mawu Ofanana  

Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa; ndipo pondiona diso, linandichitira umboni.


Ndinawasankhira njira yao ndi kukhala mkulu wao. Ndinakhala ngati mfumu mwa ankhondo ake, ngati wotonthoza ofedwa.


Taona iwe walangiza aunyinji, walimbitsa manja a ofooka.


Koma tsopano chakufikira iwe, ndipo ukomoka; chikukhudza, ndipo uvutika.


Yehova agwiriziza onse akugwa, naongoletsa onse owerama.


Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.


Mau oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva.


Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.


Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.


kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.


Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito;


Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.


Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa