Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 4:3 - Buku Lopatulika

3 Taona iwe walangiza aunyinji, walimbitsa manja a ofooka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Taona iwe walangiza aunyinji, walimbitsa manja a ofooka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Taona, iwe waphunzitsa anthu ambiri, walimbitsa mtima anthu ofooka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri, momwe walimbitsira anthu ofowoka.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 4:3
21 Mawu Ofanana  

Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.


nasunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele.


Koma ndikadakulimbikitsani ndi m'kamwa mwanga, ndi chitonthozo cha milomo yanga chikadatsitsa chisoni chanu.


Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa; ndipo pondiona diso, linandichitira umboni.


Ndinali maso a akhungu, ndi mapazi a otsimphina.


Ndinali atate wa waumphawi; ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwe ndinafunsitsa.


Anthu anandimvera, nalindira, nakhala chete, kuti ndiwapangire.


Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa, walimbitsanso maondo otewa.


Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri; koma zitsiru zimafa posowa nzeru.


Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru, koma mtima wa opusa suli wolungama.


Wanzeru mtima adzatchedwa wochenjera; ndipo kukoma kwa milomo kuonjezera kuphunzira.


Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.


Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.


Popeza mwamvetsa chisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetse chisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yake yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;


Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.


koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.


Ndipo anamuonekera Iye mngelo wa Kumwamba namlimbitsa Iye.


Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.


Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao.


Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.


Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa