Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 3:4 - Buku Lopatulika

4 Tsiku lija likhale mdima; Mulungu asalifunse kumwamba, ndi kuunika kusaliwalire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Tsiku lija likhale mdima; Mulungu asalifunse kumwamba, ndi kuunika kusaliwalire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsiku limenelo lisanduke lamdima. Mulungu kumwambako asaliganizirenso tsiku limenelo, kuŵala kusadzaonekenso pa tsikulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsiku limenelo lisanduke mdima; Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso; kuwala kusaonekenso pa tsikulo.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 3:4
9 Mawu Ofanana  

Litayike tsiku lobadwa ine, ndi usikuwo udati, Waima naye mwana wamwamuna.


Mdima ndi mthunzi wa imfa ziliyese laolao; mtambo ulikhalire; zonse zodetsa usana bii ziliopse.


tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.


Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova? Mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? Ndilo mdima, si kuunika ai.


Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.


Ndipo m'mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalire masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng'ono anatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuke chidatichokera pomwepo.


ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo chikhalire, kuyambira chaka mpaka kutsiriza chaka.


Ndipo wachisanu anatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chilombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa