Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 26:3 - Buku Lopatulika

3 Wampangira bwanji wopanda nzeruyu! Ndi kudziwitsa nzeru zenizeni mochuluka!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Wampangira bwanji wopanda nzeruyu! Ndi kudziwitsa nzeru zenizeni mochuluka!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kodi wandilangiza zabwino ine, munthu wopanda nzerune ngati? Kodi wandiwuza nzeru zambiri pamenepa ngati?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru! Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka!

Onani mutuwo Koperani




Yobu 26:3
17 Mawu Ofanana  

Zoonadi inu ndinu anthu, ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.


Koma inenso ndili nayo nzeru monga inu. Sindingakuchepereni; ndani sadziwa zonga izi?


Mwenzi mutakhala chete konse, ndiko kukadakhala nzeru zanu.


Koma bwerani inu nonse, idzani tsono; pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.


Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu. Kulipulumutsa dzanja losalimba!


Wafotokozera yani mau? Ndi mzimu wa yani unatuluka mwa iwe?


Maneno anga awulula chiongoko cha mtima wanga, ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.


Ngati mulibe mau, tamverani ine; mukhale chete, ndipo ndidzakuphunzitsani nzeru.


Ndani uyu adetsa uphungu, ndi mau opanda nzeru?


Mulibe thandizo mwa ine ndekha; chipulumutso chandithawa.


kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba zanu,


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa