Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 22:3 - Buku Lopatulika

3 Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako kuti iwe ndiwe wolungama? Kapena kodi apindula nako kuti ukwaniritsa njira zako?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako kuti iwe ndiwe wolungama? Kapena kodi apindula nako kuti ukwaniritsa njira zako?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kodi Mphambe angapeze bwino chifukwa cha kulungama kwako? Kodi kapena Iyeyo nkupindulapo kanthu pa makhalidwe ako angwirowo?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama? Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?

Onani mutuwo Koperani




Yobu 22:3
20 Mawu Ofanana  

Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.


Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire? Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?


Kodi munthu apindulira Mulungu? Koma wanzeru angodzipindulira yekha.


Kodi akudzudzula, nadza nawe kumlandu, chifukwa cha kumuopa kwako?


Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako kuvomerezana naye Mulungu.


Mukakhala wolungama, mumninkhapo chiyani? Kapena alandira chiyani padzanja lanu?


Ndinaganizira njira zanga, ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.


Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.


Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.


Okhota mtima anyansa Yehova; koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.


Milomo yonama inyansa Yehova; koma ochita ntheradi amsekeretsa.


Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.


Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo? Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.


Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?


M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.


Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa