Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 22:10 - Buku Lopatulika

10 Chifukwa chake misampha ikuzinga. Ndi mantha akuvuta modzidzimutsa,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Chifukwa chake misampha ikuzinga. Ndi mantha akuvuta modzidzimutsa,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nchifukwa chake misamphayi yakuzinga, ndipo wadzidzimuka ndi mantha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira, nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,

Onani mutuwo Koperani




Yobu 22:10
12 Mawu Ofanana  

Mundichotsere dzanja lanu kutali, ndi kuopsa kwanu kusandichititse mantha.


M'makutu mwake mumveka zoopsetsa; pali mtendere amfikira wakumuononga.


Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo, nadzampirikitsa kumbuyo kwake.


Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga, nandizinga ndi ukonde wake.


Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa, zolingirirazo ndi chiweruzo zidzakugwiranibe.


Zokolola zao anjala azidya, azitenga ngakhale kuminga, ndi aludzu ameza chuma chao.


Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.


Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula, ndi pofika tsoka lanu ngati kamvulumvulu; pakudza kwa inu vuto ndi nsautso.


Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa