Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 2:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m'dziko, ndi kuyendayenda m'mwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m'dziko, ndi kuyendayenda m'mwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pamenepo Chauta adafunsa Satanayo kuti, “Nanganso iwe Satana, kutereku ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndakhala ndikuyendayenda ndi kumangozungulira dzikoli.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, “Kodi iwe ukuchokera kuti?” Satana anayankha Yehova kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira mʼdzikoli.”

Onani mutuwo Koperani




Yobu 2:2
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake kwa wakuka wanga Sarai.


Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m'dziko ndi kuyendayenda m'mwemo.


Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadza Satana yemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda chifukwa.


Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;


mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa