Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 19:9 - Buku Lopatulika

9 Anandivula ulemerero wanga, nandichotsera korona pamutu panga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Anandivula ulemerero wanga, nandichotsera korona pamutu panga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Iye wandilanda ulemerero wanga, wandivula chisoti chaulemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iye wandilanda ulemu wanga ndipo wandivula chipewa chaufumu pamutu panga.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 19:9
14 Mawu Ofanana  

Apita nao maphungu atawafunkhira, napulukiritsa oweruza milandu.


Apita nao, ansembe atawafunkhira, nagubuduza amphamvu.


Ndadzisokerera chiguduli kukhungu langa. Ndipo ndaipsa mphamvu yanga m'fumbi.


Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka, iwo amene atate ao ndikadawapeputsa, osawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zanga.


Munakaniza chipangano cha mtumiki wanu; munaipsa korona wake ndi kumponya pansi.


Munapasula makoma ake onse; munagumula malinga ake.


Munaleketsa kuwala kwake, ndipo munagwetsa pansi mpando wachifumu wake.


pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo.


Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma cha amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.


Korona wagwa pamutu pathu; kalanga ife! Pakuti tinachimwa.


Kunena za Efuremu, ulemerero wao udzauluka ndi kuchoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa