Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 18:8 - Buku Lopatulika

8 Pakuti aponyedwa mu ukonde ndi mapazi ake, namaponda pamatanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pakuti aponyedwa m'ukonde ndi mapazi ake, namaponda pamatanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mapazi ake omwe amloŵetsa mu ukonde, ndipo wakodwa. Tsono kuti achokemo, wagweranso m'mbuna.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mapazi ake amulowetsa mu ukonde ndipo akungoyendayenda mu ukondewo.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 18:8
18 Mawu Ofanana  

Chikakomera mfumu, chilembedwe kuti aonongeke iwo; ndipo ndidzapereka matalente a siliva zikwi khumi m'manja a iwo akusunga ntchito ya mfumu, abwere nao kuwaika m'nyumba za chuma cha mfumu.


Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamgonjetsa; koma udzagwada pamaso pake.


Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.


Pamenepo mfumu Ahasuwero inalankhula, niti kwa mkazi wamkulu Estere, Ndani uyu, ali kuti iyeyu wadzazidwa mtima wake kuti azitero?


Msampha udzamgwira kuchitendeni, ndi khwekhwe lidzamkola.


Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga, nandizinga ndi ukonde wake.


Chifukwa chake misampha ikuzinga. Ndi mantha akuvuta modzidzimutsa,


Zokolola zao anjala azidya, azitenga ngakhale kuminga, ndi aludzu ameza chuma chao.


Chimgwere modzidzimutsa chionongeko; ndipo ukonde wake umene anautcha umkole yekha mwini, agwemo, naonongeke m'mwemo.


Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautchera.


M'kulakwa kwa woipa muli msampha; koma wolungama aimba, nakondwera.


Zoipa zakezake zidzagwira woipa; adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.


Mantha ndi dzenje ndi msampha zili pa iwe, wokhala m'dziko.


Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.


Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakuvuulira m'khoka mwanga.


Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.


Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitayiko.


ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa