Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 17:4 - Buku Lopatulika

4 Pakuti mwabisira mtima wao nzeru; chifukwa chake simudzawakuza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Pakuti mwabisira mtima wao nzeru; chifukwa chake simudzawakuza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Inu mwatseka mitima yao kuti asamvetsetse bwino zanzeru, choncho musalole kuti iwowo apambane.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Inu mwatseka maganizo awo kuti asamvetse zinthu; choncho simudzawalola kuti apambane.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 17:4
10 Mawu Ofanana  

Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.


Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.


Amchotsera wokhulupirika kunena kwake. Nalanda luntha la akulu.


Iye wakupereka mabwenzi ake ku ukapolo, m'maso mwa ana ake mudzada.


Yehova wasakaniza mzimu wa kusaweruzika pakati pake; ndipo iwo asocheretsa Ejipito m'ntchito zake zonse, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pake.


Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:


Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.


monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.


Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitse nzeru ya dziko lapansi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa