Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yesaya 4:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa mu Ziyoni, ndi iye amene atsala mu Yerusalemu adzatchedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo mu Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa m'Ziyoni, ndi iye amene atsala m'Yerusalemu adzatchedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo m'Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono otsalira ku Ziyoni, amene Mulungu waŵasankha kuti akhale ndi moyo ku Yerusalemu, adzatchedwa oyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iwo amene adzatsale mu Ziyoni, amene adzatsalire mu Yerusalemu, adzatchedwa oyera, onse amene mayina awo alembedwa pakati pa anthu amoyo okhala mu Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Yesaya 4:3
33 Mawu Ofanana  

Afafanizidwe m'buku lamoyo, ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.


Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu, uyu anabadwa komweko.


Ziyoni adzaomboledwa ndi chiweruzo, ndi otembenuka mtima ake ndi chilungamo.


Tsiku limenelo Yehova wa makamu adzakhala korona wa ulemerero, ndi korona wokongola kwa anthu ake otsala:


Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasochera m'menemo.


Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israele, amene ndakunyamulani kuyambira m'mimba, ndi kukusenzani chibadwire;


Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako, Ziyoni; tavala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.


Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.


Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.


Ndipo iwo adzawatcha Anthu opatulika, Oomboledwa a Yehova; ndipo iwe udzatchedwa Wofunidwa, Mzinda wosasiyidwa.


Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; kapena kulowa m'dziko la Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.


Lamulo la Kachisi ndi ili: pamwamba paphiri malire ake onse pozungulira pake azikhala opatulika kwambiri. Taonani, limeneli ndi lamulo la Kachisi.


Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,


Koma m'phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao.


Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mzindawo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mzinda lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mzindamo.


Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.


Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.


Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha.


Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu aamuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadire Baala.


Choteronso nthawi yatsopano chilipo chotsalira monga mwa kusankha kwa chisomo.


monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.


Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.


Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;


Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.


Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.


Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Iye amene apambana adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa