Yeremiya 9:26 - Buku Lopatulika26 Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m'mtima. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m'mtima. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Ndidzalanga Aejipito, Ayuda, Aedomu, Aamoni, Amowabu ndiponso onse amene amakhala m'chipululu namameta cham'mbali. Mitundu ina yonseyi njosaumbalidwa, ngakhale banja lonse la Israele nalonso nlosaumbalidwa mu mtima.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.” Onani mutuwo |