Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 9:25 - Buku Lopatulika

25 Taonani, masiku alikudza, ati Yehova, kuti ndidzalanga onse odulidwa m'kusadulidwa kwao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Taonani, masiku alikudza, ati Yehova, kuti ndidzalanga onse odulidwa m'kusadulidwa kwao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene ndidzalanga onse oumbalidwa, amene mu mtima sasamalako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 “Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:25
17 Mawu Ofanana  

Dedani, ndi Tema, ndi Buzi, ndi onse amene ameta m'mbali mwa tsitsi;


Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala mu Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu.


Ndipo ngamira zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng'ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira kumphepo zonse iwo amene ameta m'mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao kumbali zao zonse, ati Yehova.


Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndachinena, ati Ambuye Yehova.


Momwemo ufanana ndi yani mu ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni m'munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.


popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.


Musamameta mduliro, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zanu.


Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzichepetsa, ndipo avomereza kulanga kwa mphulupulu zao;


Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a padziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani chifukwa cha mphulupulu zanu zonse.


Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m'thupimo;


koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.


Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa