Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 9:22 - Buku Lopatulika

22 Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Chauta adandiwuza kuti ndinene izi: “Mitembo ya anthu idzagwa, kuchita kuti mbwembwembwe ngati ndoŵe m'minda, ngati mitolo pambuyo pa anthu ovuna. Koma palibe amene adzaitole.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti, “ ‘Mitembo ya anthu idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda, ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola, popanda munthu woyitola.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:22
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena mu ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya.


Nati iye, Anaona chiyani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pachuma changa kosawaonetsa.


ndi thupi la Yezebele lidzakhala ngati ndowe pamunda m'dera la Yezireele, kuti sadzati, Ndi Yezebele uyu.


Akola eni nzeru m'kuchenjera kwao, ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pachabe.


kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.


amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda.


Chuma cha wolemera ndicho mzinda wake wolimba; alingalira kuti ndicho khoma lalitali.


Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako.


Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.


Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.


Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika.


Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zilombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa.


ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.


Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, nadzalakwa ndi kupalamula, iye amene aiyesa mphamvu yake mulungu wake.


Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.


ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira chuma ichi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa