Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 9:19 - Buku Lopatulika

19 Pakuti mau a kulira amveka mu Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Pakuti mau a kulira amveka m'Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Kukumveka kulira kwa Ziyoni, akuti, “Kalanga ife! Taonongeka! Manyazi aakulu atigwera. Tiyenera kusiya dziko lathu, chifukwa nyumba zathu azigwetsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti, ‘Aa! Ife tawonongeka! Tachita manyazi kwambiri! Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:19
20 Mawu Ofanana  

Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phee, mumve mau anga; inu ana aakazi osasamalira, tcherani makutu pa kulankhula kwanga.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Kodi Israele ndi mtumiki? Kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? Afunkhidwa bwanji?


Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magaleta ake ngati kamvulumvulu; akavalo ake athamanga kopambana mphungu. Tsoka ife! Pakuti tapasuka.


Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m'kamphindi.


Ndipo ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efuremu.


Kodi autsa mkwiyo wanga? Ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?


Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.


Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu, chokani, chokani, musakhudze kanthu. Pothawa iwo ndi kusochera, anthu anati kwa amitundu, Sadzagoneranso kuno.


Cholowa chathu chasanduka cha alendo, ndi nyumba zathu za achilendo.


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Tiro nyimbo ya maliro;


dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m'mwemo.


lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.


Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwachita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo.


Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu.


Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.


ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa