Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 9:17 - Buku Lopatulika

17 Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ochenjera, kuti adze;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ochenjera, kuti adze;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Muziganize bwino, muitane akazi olira maliro kuti abwere. Akaziwo akhale aja amadziŵa kwambiri kuliraŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere; itanani akazi odziwa kulira bwino.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:17
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba mu Israele; taonani, zilembedwa mu Nyimbo za Maliro.


Autemberere iwo akutemberera usana, Odziwa kuutsa Leviyatani.


inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;


Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.


Ambuye wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Tiro nyimbo ya maliro;


Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana aakazi a amitundu adzachita nayo maliro; adzalirira nayo Ejipito ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.


Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu.


Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.


Ndipo Yesu polowa m'nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma,


Ndipo anafika kunyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo anaona chipiringu, ndi ochita maliro, ndi akukuwa ambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa