Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 9:16 - Buku Lopatulika

16 Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwe; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwa; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndidzaŵabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo ao sadaidziŵe. Ndidzaŵalondola ndi ankhondo mpaka kuŵatheratu onse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:16
29 Mawu Ofanana  

Mukumbukire mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu;


Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.


inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;


Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu.


Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi mliri mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.


Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, chifukwa cha lupanga limene ndidzatumiza mwa inu.


Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.


Taonani, ndiwayang'anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.


Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele.


Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwamwaza Ine mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.


Kapena ndikadza padziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati padziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;


Ndinawakwezeranso dzanja langa m'chipululu, kuti ndidzawabalalitsa mwa amitundu, ndi kuwamwaza m'maiko;


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Tiro nyimbo ya maliro;


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.


Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.


koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.


Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.


Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.


Ndinati, Ndikadawauzira ndithu, ndikadafafaniza chikumbukiro chao mwa anthu.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.


Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa