Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 9:12 - Buku Lopatulika

12 Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupserera monga chipululu, kuti anthu asapitemo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupsereza monga chipululu, kuti anthu asapitemo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ine ndidati, “Kodi wanzeru ndani, amene angamvetse zimenezi? Chauta adazifotokozera yani, kuti iyeyo akafotokozere ena? Nanga chifukwa chiyani dziko laonongeka ndi kusanduka chipululu, m'mene anthu sapitamo?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:12
22 Mawu Ofanana  

Dziko la zipatso, likhale lakhulo, chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.


Wokhala nazo nzeru asamalire izi, ndipo azindikire zachifundo za Yehova.


Ndani mwa inu adzatchera khutu lake pamenepo? Amene adzamvera ndi kumva nthawi yakudza?


Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.


Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.


Koma akadaima mu upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao.


Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lake; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi chiyani polinganiza ndi tirigu? Ati Yehova.


Koma imvani mau a Yehova, akazi inu, khutu lanu lilandire mau a pakamwa pake, phunzitsani ana anu akazi kulira, ndi yense aphunzitse mnzake maliridwe ake.


Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichite kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova.


Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.


Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova.


Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.


Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; mizinda yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.


Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)


Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ichi, akadasamalira chitsirizo chao!


Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa