Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 7:32 - Buku Lopatulika

32 Chifukwa chake, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wa Hinomu, koma Chigwa cha Kuphera; pakuti adzataya mu Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Chifukwa chake, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wa Hinomu, koma Chigwa cha Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Nchifukwa chake nthaŵi ikubwera pamene malo ano sadzatchedwanso Tofeti, kapena za Chigwa cha Benihinomu, koma za Chigwa cha Chipheiphe, pakuti anthu akufa adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti sikudzapezekanso malo owaika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Nʼchifukwa chake masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzawatchulanso malowo Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma adzawatchula Chigwa cha Imfa, chifukwa adzakwirira anthu akufa ku Tofeti mpaka osapezekanso malo owayika.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 7:32
10 Mawu Ofanana  

Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.


nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu awa ndi mzinda uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso, ndipo adzaika maliro mu Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.


ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.


nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la Chipata cha Mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;


chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wake wa Hinomu, koma Chigwa Chophera anthu.


Ndipo chigwa chonse cha mitembo, ndi cha phulusa, ndi minda yonse kufikira kumtsinje wa Kidroni, kufikira kungodya kwa Chipata cha Akavalo kuloza kum'mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse kunthawi zamuyaya.


Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindiwanauze iwo, sichinalowe m'mtima mwanga.


Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.


Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa