Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 6:25 - Buku Lopatulika

25 Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Musayesere kupita ku minda, kapena kuyenda pa mseu, pakuti adani akubwera ndi nkhondo ndipo ponseponse pali mantha okhaokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Musapite ku minda kapena kuyenda mʼmisewu, pakuti mdani ali ndi lupanga, ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 6:25
20 Mawu Ofanana  

Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakutuluka, kapena kwa iye wakulowa, koma mavuto aakulu anagwera onse okhala m'maikomo.


Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo, nadzampirikitsa kumbuyo kwake.


Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.


koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.


Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mzinda, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.


Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.


Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'mizinda ya malinga.


Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.


Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zotchingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamira zao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse.


Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akuchokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ake, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osochera.


Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.


Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!


Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano; panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova; omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.


Inenso ndidzaomba manja anga, ndipo ndidzakukwaniritsa ukali wanga; Ine Yehova ndanena.


Ndipo adzadzimangira m'chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi.


Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa