Yeremiya 6:23 - Buku Lopatulika23 Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Atenga mauta ndi mikondo, ndi anthutu ankhalwe ndi opanda chifundo. Phokoso lao lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo, akonzekera ngati munthu wankhondo, akudzamenyana nawe, iwe Ziyoni.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Atenga mauta ndi mikondo; ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo. Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo awo ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo, kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.” Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.