Yeremiya 6:22 - Buku Lopatulika22 Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu udzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu adzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Chauta akunena kuti, “Onani, anthu a mtundu wina akubwera kuchokera ku dziko lakumpoto. Mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka kuchokera mbali zakutalitali za dziko lapansi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Yehova akunena kuti, “Taonani, gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto; mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.