Yeremiya 6:21 - Buku Lopatulika21 Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Nchifukwa chake anthu ameneŵa ndidzaŵaikira zoŵakhumudwitsa. Atate ndi ana ao aamuna, anansi ndi abwenzi ao, onsewo adzaonongeka.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Choncho Yehova akuti, “Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa. Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa; anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.” Onani mutuwo |
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.