Yeremiya 6:11 - Buku Lopatulika11 Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa misonkhano ya anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Nchifukwa chake ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Chauta, sindingathenso kudzimanga kuti usatulukire kunja. Chauta akuti, “Mkwiyo umenewu ukauthire pa ana oyenda mu mseu, ndi pa achinyamata kumene amasonkhanira. Mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, ngakhale aimvi ndi okalamba kwambiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova, ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova. Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi; pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka. Onani mutuwo |