Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 52:8 - Buku Lopatulika

8 Koma nkhondo ya Ababiloni inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m'zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yake yonse inambalalikira iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma nkhondo ya Ababiloni inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m'zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yake yonse inambalalikira iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma gulu lankhondo la Ababiloni lidamlondola mfumu Zedekiya nkukamgwirira m'zigwa za ku Yeriko. Ankhondo ake adabalalika namsiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 52:8
13 Mawu Ofanana  

Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.


ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;


Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ake ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, imene yakuchokerani.


pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni.


Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndachimwira inu chiyani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende?


Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mzindawu ndi moto.


Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa