Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 52:6 - Buku Lopatulika

6 Mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, njala inavuta m'mzinda, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, njala inavuta m'mudzi, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono pa tsiku lachisanu ndi chinai, pa mwezi wachinai wa chaka chimenecho, pamene njala inali itakula kwambiri mumzindamo kotero kuti anthu analibiretu chakudya m'dzikomo,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti munalibe chakudya choti anthu nʼkudya.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 52:6
23 Mawu Ofanana  

Tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi wachinai njala idakula m'mzindamo, panalibe chakudya kwa anthu a m'dzikomo.


Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo;


Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.


Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.


Iye amene akhala m'mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.


Ndiponso ndidzawachotsera mau akusekera ndi mau akukondwera, ndi mau a mkwati, ndi mau a mkwatibwi, mau a mphero, ndi kuwala kwa nyali.


Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mzinda. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.


Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mzindamu.


Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mzinda unabooledwa.


Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.


Khungu lathu lapserera ngati pamoto chifukwa cha kuwawa kwa njala.


Likandichimwira dziko ndi kuchita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulithyolera mchirikizo wake, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,


Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?


Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi wachitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,


Pakuwatumizira Ine mivi yoipa ya njala yakuononga, imene ndidzatumiza kukuonongani, pamenepo ndidzakukuzirani njala, ndi kukuthyolerani mchirikizo, ndiwo chakudya.


Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mzindawo njala ndi mliri zidzamutha.


Pamene ndithyola mchirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mchembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.


Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.


Adzaonda nayo njala adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa; ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo, ndi ululu wa zokwawa m'fumbi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa