Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 52:30 - Buku Lopatulika

30 chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Nebukadinezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Nebukadinezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Pa chaka cha 23 cha ufumu wa Nebukadinezara, Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda oteteza mfumu uja adatenga ukapolo Ayuda 745. Onse pamodzi otengedwa ukapolo adakwanira 4,600.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara, Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo a mfumu anagwira Ayuda 745 kupita ku ukapolo. Onse pamodzi analipo anthu 4,600.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 52:30
6 Mawu Ofanana  

Ndi anthu otsalira m'mzinda, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babiloni, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkulu wa olindirira anamuka nao andende.


Ndipo mwezi wachisanu, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo, ndicho chaka chakhumi mphambu chisanu ndi chinai cha mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, Nebuzaradani mkulu wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babiloni, anadza ku Yerusalemu,


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni.


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mzinda, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babiloni, ndi otsala a unyinjiwo.


chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara iye anatenga ndende kuchokera mu Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri;


Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa