Yeremiya 52:25 - Buku Lopatulika25 ndipo m'mzinda anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mzinda; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makamu asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mzinda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makamu asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Mumzindamo adagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndiponso anthu asanu ndi aŵiri amene anali aphungu a mfumu mumzindamo. Adagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu am'dzikomo, ndiponso akuluakulu ena 60, amene anali mumzindamo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Mu mzindamo anagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndi alangizi amfumu asanu ndi awiri. Anagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu mʼdzikomo, pamodzi ndi anthu ena 60 amene anali mu mzindamo. Onani mutuwo |