Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 52:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pake; utali wake wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi sefa ndi makangaza pakorona pozungulira pake, onse amkuwa: nsanamira inzake yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pake; utali wake wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi sefa ndi makangaza pakorona pozungulira pake, onse amkuwa: nsanamira inzake yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Inali ndi mutu wamkuŵa, kutalika kwake mamita aŵiri. Pozungulira mutuwo panali ukonde ndi makangaza, zonsezo zamkuŵa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangaza ndipo inkafanana ndi inzakeyo pa zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Pamwamba pa nsanamira iliyonse panali mutu wamkuwa umene kutalika kwake kunali mamita awiri. Pozungulira pake panali ukonde ndi makangadza, zonsezo za mkuwa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangadza ake ndipo inali yofanana ndi inzake ija.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 52:22
9 Mawu Ofanana  

Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwake mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga ndanda mutu winawo.


ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,


Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.


Ndipo anapanga ku khomo la nyumba nsanamira ziwiri za mikono makumi atatu mphambu ziwiri; ndi mutu unakhala pamwamba pa iliyonse ndiwo mikono isanu.


Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa