Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 52:17 - Buku Lopatulika

17 Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, nanka nao mkuwa wake wonse ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, nanka nao mkuwa wake wonse ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Ankhondo a ku Babiloni adaphwanya nsanamira zamkuŵa za m'Nyumba ya Chauta, ndiponso maphaka ndi chimbiya chamkuŵa, ndipo adatenga mkuŵa wonsewo, napita nawo ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ababuloni anaphwanya nsanamira za mkuwa, maphaka ndi chimbiya chamkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova. Anatenga mkuwa wonsewo nʼkupita nazo ku Babuloni.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 52:17
12 Mawu Ofanana  

ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira moto za golide woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolide, za zitseko za chipinda cha m'katimo, malo opatulika kwambiri, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kachisi.


Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kunka ku Babiloni, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.


Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.


Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomoni anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanathe kuyesa kulemera kwake.


Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.


M'litali mwake mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi chakuno, ndi imodzi chauko.


Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa