Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 52:1 - Buku Lopatulika

1 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza chimodzi pamene analowa ufumu wake; ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka khumi kudza chimodzi; dzina la amake ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza chimodzi pamene analowa ufumu wake; ndipo analamulira m'Yerusalemu zaka khumi kudza chimodzi; dzina la amake ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya wa ku Libina.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Zedekiya anali wa zaka 21 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 52:1
12 Mawu Ofanana  

Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu miyezi itatu mu Yerusalemu ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.


Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.


Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iye ndi khamu lake lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.


Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi.


Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi,


Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asiriya ilikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inachoka ku Lakisi.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,


Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse ku Yerusalemu, ndi kuumangira misasa.


Mau amene Yeremiya mneneri anauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babiloni chaka chachinai cha ufumu wake. Ndipo Seraya anali kapitao wa chigono chake.


Kodi m'mwemo adzakhuthula mu ukonde mwake osaleka kuphabe amitundu?


Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye anapitirira kuchokera ku Makeda kunka ku Libina, nathira nkhondo pa Libina;


Libina ndi Eteri ndi Asani;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa