Yeremiya 51:62 - Buku Lopatulika62 nuti, Inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201462 nuti, Inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa62 Ukanene kuti, ‘Inu Chauta, mwalengeza cholinga chanu chofuna kuwononga malo ano, osasiyapo kanthu, munthu kapena nyama. Ndipo adzakhala chipululu mpaka muyaya.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero62 Ndipo ukanene kuti, ‘Inu Yehova, mwanena kuti mudzawononga malo ano, kotero kuti simudzatsala munthu kapena nyama mʼdziko muno; lidzakhala chipululu mpaka muyaya.’ Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.